• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sun05192013

Last update09:34:28 AM

Back Malawi News Headlines Tikambe Mabungwe awawuza apeze njira zambiri zopezera chithandizo

Mabungwe awawuza apeze njira zambiri zopezera chithandizo

Mabungwe omwe siaboma m'dziko akhoza kukhala pachiopso chachikulu cholephera kupitiliza ntchito zachitukuko ngati adalira njira imodzi yopezera thandizo monga ndalama zochokera kwa anthu akufuna kwabwino kapena mabungwe akumaiko akuja.

Izi zidayankhulidwa ndi bungwe lina lowona za ufulu wa ana pa maphunziro m'dziko muno la Education Expertise Development Foundation (EEDF) pa maphunziro a momwe mabungwe angapezere njira zochuluka zopezera thandizo. Maphunzirowo, omwe adali ndi nthu oyimila mabungwe oposa 10, adachitikira pa hotela ya Kambiri m'boma la Salima sabata latha.

Ndipo mabungwe omwe adatengapo mbali pa mabunzirowo ndi okhawo amene ali ndi nthambi ya maphunziro mu ntchito zake zachitukuko komaso kulandila chithandizo ku abwenzi komaso mabungwe aku Holland ngati Edukans.

"Pali chiopsezo chachikulu chomwe chingalepheletse kupitiliza ntchito zachitukuko pakati pa mabungwe omwe siaboma ngati mabungwewo sakhala ndi njira zambiri zodalilika zopezera thandizo. Izi zingakhale chomwechi kaamba koti mabungwe ena amadalira njira imodzi yopezera chithandizo kotero kuti akhoza kuvutika zitakhala mukuti njirayi yasokonekera," adatero a Robert Mponela, omwe ndi mkulu wa bungwe la EEDF.

Iwo adafotokoza kuti chithandizo chomwe bungwe kuphatikizapo anthu akufuna kwabino akumaiko akunja amapeleka kwa mabungwe ene m'dziko muno chikunka chikutsika. Kotero kuti pofika mchaka cha 2015 mabungwe ena adzakhalilatu opanda thandizo.

"Kweni kweni chomwe tikufuna ndichakuti mabungwe omwe siaboma akhala ndi ndondomeko yomwe pachingerezi tikuyitchula kuti Resource Mobilisation Strategy (RMS) ndicholinga choti akhale odzidalira paokha," adatero a Mponela.

Mwa ena mwamabungwe omwe adatengapo gawo pa maphunzirowo ndi monga Samaritan Trust, Good News Revival Community Development Services (GOCODES), Livingstonia Synod of the CCAP, Word Alive Ministries.

Ndipo m'mawu ake a Ritchard Luhanga ogwira ntchito mu nthambi ya zamaphunziro mu Synod ya Livingstonia adati maphunzirowo adali opindula kwambiri ndipo kuti akathandiza kutukula ntchito zopezera thadizo za Livingstonia Synod.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com