• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sun05192013

Last update01:14:09 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Gogo akusalidwa kaamba ka ukalamba

Gogo akusalidwa kaamba ka ukalamba

Gogo_NyamuNyirenda

Kwa anthu ena ukalamba ndi nthawi yosangalala pozungulidwa ndi zidzukulu komanso kusangalala ndi mathandizo ochoka kwa ana omwe anabeleka. Koma kwa Gogo Esther NyamuNyirenda ukalamba ndi malodza popeza alibe zidzukulu komanso akusowa thandizo la tsiku ndi tsiku komanso anthu ena akuwasala.

Izi zili chomwecho kaamba kakuti amuna awo ndi ana [atatu] onse anatsikira kulichete. Gogo'yu yemwe akuti pamene nkhondo ya chiwiri ya dziko lonse inkachitika anali mtsikana wachichepere ndipo sakukumbukira zaka zake zobadwa.

Gogoyu akuchokera m'mudzi mwa Hwati Mvalo mfumu yaikulu Mankhunikira m'boma la Rumphi.

Zokhoma zomwe akukumana nazo

Gogoyu adauza Tikambe kuti pa ukalamba wake komanso umasiye wake akukumana ndi zokhoma zambiri.

"Ndilibe nyumba yodalirika kaamba kakuti kanyumba komwe ndimakhala ndi kamitengo ya fodya komanso komata kotero kamagwaigwa, mwinanso denga limasasulidwa ndi mphepo.

"Ndikuyamika anthu achifundo omwe amandithandiza vutoli likandionekera," Gogo Nyirenda anatero

Chinanso gogo'yu akuti akusowa ndalama yogulira zovala ndi zofunikira zina mnyumba monga ziwiya.

"Ndine bwenzi la njala, ngakhale kuti ndinalima chimanga koma sichokwanira malinga ndi kuperewera kwa mphamvu.

"Ndimagona osafunda popeza ndiribe chofunda choncho ndimadwala chibayo pafupipafupi nthawi ya chisanu'yi.

"Ndimavutika kwambiri pakakhala kuti palibe wondizonda kunditengera ku chipatala," Gogoyu adadandaula.

Iye adapitiriza kufotokoza kuti malinga ndi ukalamba wake amavutika kuphika ndipo ngakhale akhale ndi njala amasowa chochita ngati anthu akufuna kwabwino sawathandiza.

"Nthawi zambiri ndimagona ndi njala kaamba kukuti ndimakanika kuphika komanso madzi sindingathe kutunga ndekha.

"Koma anthu akufuna kwabwino amatha kundithandiza ngakhale kuti ena amandinyoza pomati ana anga ndi abale anga ndidapha dala ndekha ndiye chifukwa chake ndikuvutika," gogoyu adatero.

Mpingo sukukhala chete

Mpingo sikukhala chete pa vuto lomwe gogo Nyilenda akukumana nalo, ndipo Tikambe idacheza ndi m'busa Patson Mgala wa CCAP ku Mzokoto yemwenso ndi wa chiwiri kwa mlembi wa Presbytery la Rumphi omwe adati gogoyu amamuthandiza pa moyo wa uzimu.

"Gogoyu ndi mkhirisitu wathu kotero timamuyendera ndikumamulimbikitsa moyo wa uzimu.

"Pa moyo wa uzimu aliyense ayenera kutenga gawo, ndipo anthu okalamba ali gulu la anthunso kotero sitiyenera kuwasala.

"Komanso malinga ndi ndondomeko, a khristu amapereka zinthu ku mpingo monga zokolola za mbewu zosiyanasiyana, ndalama kapena zovala ku mpingo kuthokoza namalenga mwini zonse.

"Katunduyi akasonkhanitsidwa amagawidwa kwa anthu okalamba, osowa kapena amasiye," m'busa Mgala anatero.

Mafumu nawonso akuyesetsa kuthandizapo.

Mfumu Hwati Mvalo aku Rumphi adauza Tikambe kuti mafumu anagundana mitu pa nkhani ya mmene angathamandizire anthu okalamba komanso gogo'yu.

"Ife mafumu tidakumana ndipo tidauza anthu athu kuti munthu aliyense m'mudzi azikhala ndi mtima wothandiza anthu osowa komanso okalamba.

"Koma chachikulu ndi chakuti mafumu'fe tikhale patsogolo kuthandiza anthu ngati gogoyu kuti anthu athu adzitengera chitsanso chabwino.

"Anthu okalamba sadasankhe kukhala chomwecho, komanso ndikulakwa kumanyoza anthu okalamba pomawanena kuti ndi mfiti komanso kuti adapha ana awo," a Mvalo adatero.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com