Chipatso kapena mbewu iliyonse makamaka chimanga chikafika podyeka amati chakhwima, koma mawu omwewo kumunena wina kuti "wokhwima iwe" amadana nazo kaamba koti amawona ngati wamuyalutsa, ndiye pali ena amakhwimira katundu, nanga zikusiyana pati? Nyakwawa Nzeru ya m'boma la Blantyre ikufotokoza kusiyana kwake motere:
Kodi kukhwima kumathandiza chiyani?
Poyamba zimene tikambe pano ndi zimene makolo athu ankachita, komabe ngati alipo ena akuchitabe izo nzawo. Munthu akakhwima amadana kwambiri ndi afiti chifukwa amalephera akabwera kudzamutambira, kumuyesa umu ndi umu, pambuyo pake amadana naye amvekere wokhwima iwe. Osadziwa kuti alephera kuponya matsenga osiyanasiyana kuti amulodze. Pamafika pena pake akamulephera mangowonera ukakumana naye pa njira kuyang'ana kumbali, mwina angomvera mtsonyo twii; kenako amawuzana kuti uje wokhwima. Nthawi zambiri anthu akafuna kunena zining'a zawo amati "mkulu uyu" osafuna kunena poyera kuti ndi wokhwima kumakhala kuphiphiritsa kuti ana asadziwepo kanthu.
Zimayenda bwanji, kodi amatemera thupi lonse?
Ayi, pali njira zambiri zimene asing'anga ena amachita akafuna kumukhwimitsa munthu ena amamutengera pa chulu kuti pamene agang'a (chiswe chachikulu) chikamamuluma sing'anga azipakamo mankhwala mmalo motema mphini, ndiye pali ena amangotema monga nthawi zonse. *Bwinotu ndatitu akuti nthawiyo zimakhala choncho. Kukhwima kumathandiza, makolo kalelo ankati akamanga zitaganya amakonda kutsirika mudzi kuti afiti asamatambire mbumba zawo. Choncho kutsirika kwa mudziko timati kukhwimira mudzi, kotero kuti ngakhale afiti ayesere umu ndi umu kutambira mbumba zake osachita kanthu.
Nanga kusiyana kwa kukhwimira ndi kukhwima kuli pati?
Kukhwima ndi kuteteza thupi mwina ndidakangoti kutsirika thupi, pamene ena amakhwimira mbumba ndi ulemelero.
Mwachitsanzo; pali anthu ena amene ali ndi sitolo, zigayo, galimoto makamaka minibasi atha kukhwimira chuma kuti afiti kapena amatsenga akati amuchite chipongwe azilephera makamaka akakhala kuti ali ndi sitolo. Nthawi zina munthu amatha kukhwimira khola kaya ndi la ng'ombe, nkhumba kapena mbuzi mwakuti kukabwera fisi kapena mbava osaliwona kholalo, koma kuyipa kwake mudzapeza kuti khola loterelo kupha nyama yake simakoma monga nyama zina zonse; kusonyeza kuti zizimba za kholalo ndi zachabe. Mwina inunso tsiku lina mudamvapo munthu wina atagula nyama kaya ya mbuzi kapena nkhumba ngakhale ng'ombe yochokera m'khola lotsirikidwa kuphika nyama yake osakoma, kusonyeza kuti adachitira zizimba zoyipa.
Mpaka kukhwimira chigayo?
Eee! Za ife achikuda ndi zovuta kuzimvetsa, chifukwa zidachokera kumakolo, choncho safuna kuzisiya kwa iwo amati "kulemekeza mizimu ya makolo". Munthu atha kugula chigayo chatsopano koma kumangojombajomba, wina chigayo chakalekale koma osajomba. Wina sitolo kudzadzitsa katundu koma osawona kumene kukupita ndalama zake.
Mwachitsanzo; mkulu wina ku Chikhwawa atagula chigayo chake, sing'anga adamuwuza kuti aphe mdzukulu wake kuti akhale m'chigayomo, ndipo zinthu zidayamba kumuyendera; chigayo osajombajomba, komanso anthu odzagayitsa amachuluka. Koma vuto lake zinthu zokhwimira zimakhala ndi nthawi yake, ngati sing'anga adakuwuza kuti utha zaka zisanu zimakhala zomwezo, mukuwawonawa amayendera zaka....
Kodi kukhwima amachitiranso zizimba...?
Ayi akakutemera kapena akakusambitsa basi zathera pomwepo, pamene kukhwima pamafunika zizimba; kaya kuphera mdzukulu kapena kudzipha wekha.
Mukati kudzipha wekha mukutanthawuzanji?
Nthawi zina sing'anga atha kukutemera kuti ulemere amakuwuza kuti ukagone ndi mayi ako kapena achemwali ako, ndipo ukapanda kutero upenga misala, ndiye pali ena amamuwuza munthu kuti azichotse "mphamvu" m'thupi.
Asing'anga ena amamuwuza munthu kuti mkazi wake akakhala ndi pakati azichotsa mimba komwe kumakhala kudyetsera zizimba.
Mwachidule; kuyipa kokhwimira chuma kumazunza munthu kaamba koti amakhala ndi nkhawa ndipo amasowa mtendere, koti ngakhale macheza akome chotani amada nkhawa pokumbukira zizimba zimene sing'anga adamuwuzira.
Taganizani; sing'anga akuwuze kuti tsiku lililonse mbandakucha ali mbulanda azizungulira nyumba, (ndiye mmene timakomera tulo muja...), kapena mmawa uliwonse usananyamuke kupita kugeni azitenga mbamu nkususa ku malo obisika kwa mkazi wako.... Ndiye pali ena mmalo mophera munthu amawuzidwa kuti alembe wantchito ndipo ampusitse chikhale ngati chizimba kuti akamayendayenda mumsewu bizinesi iziyenda bwino. Inunso mwawonapo anthu ena "alunga" amene amanka nazungulira m'tawuni kupempha, ndiye pali ena kupempha kwawo ndi K5 basi, zonsezo zimakhala zizimba....

Advertisement







